UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.89 kB
["Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.","Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.","Chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima.","Mtima wa anzeru uli m'nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m'nyumba ya kuseka.","Kumva chidzudzulo cha anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru.","Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe.","Indetu nsautso uyalutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima.","Chitsiriziro cha kanthu chiposa chiyambi chake; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima.","Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'chifuwa cha zitsiru.","Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.","Nzeru ili yabwino pamodzi ndi cholowa; akuona dzuwa apindula nayo.","Pakuti nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.","Tapenya ntchito ya Mulungu; pakuti ndani akhoza kulungamitsa chomwe iye anachikhotetsa?","Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ichi pambali pa chinzake, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao.","Ndaona zonsezi masiku anga achabe; pali wolungama angofa m'chilungamo chake, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwake.","Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziononga wekha?","Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?","Kuli kwabwino kugwira ichi; indetu, usachotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzatuluka monsemo.","Nzeru ilimbitsa wanzeru koposa akulu khumi akulamulira m'mudzi.","Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.","Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera;","pakuti kawirikawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.","Ndayesa zonsezi ndi nzeru; ndinati, Ndidzakhala wanzeru; koma inanditalikira.","Chakutali ndi chakuyadi, adzachipeza ndani?","Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;","ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.","Taonani, ichi ndachipeza, ati Mlalikiyo, m'kuphatikiza chinthu china ndi chinzake, ndikazindikire malongosoledwe ao;","chomwe moyo wanga uchifuna chifunire, koma osachipezai ndi ichi, mwamuna mmodzi mwa chikwi ndinampezadi, koma mkazitu mwa onsewo sindinampeza.","Taonani, ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu."]