UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.38 kB
["Pali choipa ndachiona kunja kuno chifalikira mwa anthu,","munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa.","Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;","pakuti ikudza mwachabe, nichoka mumdima, mdima nukwirira dzina lake.","Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma;","akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita kumalo amodzi?","Ntchito zake zonse munthu angogwirira m'kamwa mwake, koma mtima wake sukhuta.","Pakuti wanzeru ali ndi chiyani choposa chitsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pamaso pa amoyo ali ndi chiyani?","Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.","Chomwe chinalipo chatchedwa dzina lake kale, chidziwika kuti ndiye munthu; sakhoza kulimbana ndi womposa mphamvu.","Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji?","Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?"]