bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.7 kB
JSON
["Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo;","ngakhale lisanade dzuwa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula;","tsikulo omwe asunga nyumba adzanthunthumira, amuna olimba nadzawerama, akupera nadzaleka poperewera, omwe ayang'ana pamazenera nadzadetsedwa;","pa khomo lakunja padzatsekeka; potsika mau akupera, wina nanyamuka polira mbalame, ndipo akazi onse akuimba sadzamveka bwino;","inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;","chingwe chasiliva chisanaduke, ngakhale mbale yagolide isanasweke, ngakhale mtsuko usanaphwanyike kukasupe, ngakhale njinga yotungira madzi isanathyoke kuchitsime;","fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.","Chabe zachabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi chabe.","Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri.","Mlalikiyo anasanthula akapeze mau okondweretsa, ndi zolemba zoongoka ngakhale mau oona.","Mau a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mau amene mbusa mmodzi awapatsa mau ao akunga misomali yokhomedwa zolimba.","Pamodzi ndi izi, mwananga, tachenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.","Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.","Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa."]