UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.69 kB
["Mwananga, ngati waperekera mnzako chikole,ngati wapangana kulipirira mlendo,","wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako,wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako.","Chita ichi tsono; mwananga, nudzipulumutse;popeza walowa m'dzanja la mnzako,pita nudzichepetse, numdandaulire mnzako.","Usaone tulo m'maso mwako,ngakhale kuodzera zikope zako.","Dzipulumutse wekha ngati mphoyo kudzanja la msaki,ndi mbalame kudzanja la msodzi.","Pita kunyerere, waulesi iwe,penya njira zao nuchenjere;","zilibe mfumu,ngakhale kapitao, ngakhale mkulu;","koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe;nizituta dzinthu zao m'masika.","Udzagona mpaka liti, waulesi iwe?Udzauka kutulo tako liti?","Tulo ta pang'ono, kuodzera pang'ono,kungomanga manja pang'ono, ndi kugona;","ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala,ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.","Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu;amayenda ndi m'kamwa mokhota.","Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake,amalankhula ndi zala zake;","zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka;amapikisanitsa anthu.","Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka;adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.","Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida;ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa:","Maso akunyada, lilime lonama,ndi manja akupha anthu osachimwa;","mtima woganizira ziwembu zoipa,mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu;","mboni yonama yonong'ona mabodza,ndi wopikisanitsa abale.","Mwananga, sunga malangizo a atate wako,usasiye malamulo a mai ako;","uwamange pamtima pako osaleka;uwalunze pakhosi pako.","Adzakutsogolera ulikuyenda,ndi kukudikira uli m'tulo,ndi kulankhula nawe utauka.","Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika;ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.","Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa,ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere.","Asakuchititse kaso m'mtima mwako,asakukole ndi zikope zake.","Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama,udzamaliza ndi nyenyeswa;ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengo wapatali.","Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake,osatentha zovala zake?","Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka,osapsa mapazi ake?","Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake;womkhudzayo sadzapulumuka chilango.","Anthu sanyoza mbala ikaba,kuti ikhutitse mtima wake pomva njala;","koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri;idzapereka chuma chonse cha m'nyumba yake.","Wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru;wofuna kuononga moyo wakewake ndiye amatero.","Adzalasidwa nanyozedwa;chitonzo chake sichidzafafanizidwa.","Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna,ndipo sadzachitira chifundo tsiku lobwezera chilango.","Sadzalabadira chiombolo chilichonse,sadzapembedzeka ngakhale uchulukitsa malipo."]