UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.31 kB
["Iyinso ndiyo miyambo ya Solomoniimene anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda anailemba.","Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu;koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu.","Pamlengalenga patalika, ndi padziko pakuya,koma mitima ya mafumu singasanthulike.","Chotsera siliva mphala yake,mmisiri wa ng'anjo atulutsamo mbale.","Chotsera woipa pamaso pa mfumu,mpando wake udzakhazikika m'chilungamo.","Usadzitame pamaso pa mfumu,ngakhale kuima m'malo mwa akulu.","Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno,kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga,amene maso ako anamuona.","Usatuluke mwansontho kukalimbana,ungalephere pa kutha kwake,atakuchititsa mnzako manyazi.","Nena mlandu wako ndi mnzako,osawulula zinsinsi za mwini;","kuti wakumva angakutonze,mbiri yako yoipa ndi kusachoka.","Mau oyenera a pa nthawi yakeakunga zipatso zagolide m'nsengwa zasiliva.","Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka,momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.","Monga chisanu cha chipale chofewa pa nthawi ya masika,momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma;atsitsimutsa moyo wa ambuyake.","Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula,momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga.","Chipiriro chipembedza mkulu;lilime lofatsa lithyola fupa.","Wapeza uchi kodi? Idyapo wokwanira,kuti ungakukole, nusanze.","Phazi lako lilowe m'nyumba ya mnzako kamodzikamodzi;kuti angatope nawe ndi kukuda.","Wochitira mnzake umboni wonamandiye chibonga, ndi lupanga, ndi muvi wakuthwa.","Kukhulupirira munthu wa chiwembu tsiku latsokakunga dzino lothyoka ndi phazi loguluka.","Monga wovula malaya tsiku lamphepo,ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda,momwemo woimbira nyimbo munthu wachisoni.","Mdani wako akamva njala umdyetse,akamva ludzu ummwetse madzi.","Pakuti udzaunjika makala amoto pamtu pake;ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.","Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula;chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.","Kukhala pangodya ya tsindwi kufunikakuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.","Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa,momwemo mau abwino akuchokera kudziko lakutali.","Monga kasupe wopondedwa, ndi chitsime choonongeka,momwemo wolungama ngati agonjera woipa.","Kudya uchi wambiri sikuli kwabwino;chomwecho kufunafuna ulemu wakowako sikuli ulemu.","Wosalamulira mtima wakeakunga mudzi wopasuka wopanda linga."]