bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.47 kB
JSON
["Mwananga, ukalandira mau anga,ndi kusunga malamulo anga;","kutcherera makutu ako kunzeru,kulozetsa mtima wako kukuzindikira;","ukaitananso luntha,ndi kufuulira kuti ukazindikire;","ukaifunafuna ngati siliva,ndi kuipwaira ngati chuma chobisika;","pompo udzazindikira kuopa Yehovandi kumdziwadi Mulungu.","Pakuti Yehova apatsa nzeru;kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m'kamwa mwake.","Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni;ndiye chikopa cha oyenda molunjika;","kuti atchinjirize njira za chiweruzo,nadikire khwalala la opatulidwa ake.","Pamenepo udzazindikira chilungamo ndi chiweruzo,zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.","Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako,moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,","kulingalira kudzakudikira,kuzindikira kudzakutchinjiriza;","kukupulumutsa kunjira yoipa,kwa anthu onena zokhota;","akusiya mayendedwe olungama,akayende m'njira za mdima;","omwe asangalala pochita zoipa,nakondwera ndi zokhota zoipa;","amene apotoza njira zao,nakhotetsa mayendedwe ao.","Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere,kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake;","wosiya bwenzi la ubwana wake,naiwala chipangano cha Mulungu wake.","Nyumba yake itsikira kuimfa,ndi mayendedwe ake kwa akufa;","onse akunka kwa iye sabweranso,safika kunjira za moyo;","nzeru idzakuyendetsa m'njira ya anthu abwino,kuti usunge mayendedwe a olungama.","Pakuti oongoka mtima adzakhala m'dziko,angwiro nadzatsalamo.","Koma oipa adzalikhidwa m'dziko,achiwembu adzazulidwamo."]