bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.8 kB
JSON
["Wopanduka afunafuna chifuniro chake,nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.","Wopusa sakondwera ndi kuzindikira;koma kungovumbulutsa za m'mtima mwake.","Pakudza wamphulupulu padzanso kunyoza;manyazi natsagana ndi chitonzo.","Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya;kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.","Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankho sikuli kwabwino,ngakhale kuchitira chetera wolungama.","Milomo ya wopusa ifikitsa makangano;ndipo m'kamwa mwake muputa kukwapulidwa.","M'kamwa mwa wopusa mumuononga,milomo yake ikhala msampha wa moyo wake.","Mau akazitape akunga zakudya zolongosoka,zotsikira m'kati mwa mimba.","Wogwira ntchito mwaulesindiye mbale wake wa wosakaza.","Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba;wolungama athamangiramo napulumuka.","Chuma cha wolemera ndicho mudzi wake wolimba;alingalira kuti ndicho khoma lalitali.","Mtima wa munthu unyada asanaonongeke;koma chifatso chitsogolera ulemu.","Wobwezera mau asanamvetse apusa,nadzichititsa manyazi.","Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala;koma ndani angatukule mtima wosweka?","Mtima wa wozindikira umaphunzira;khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.","Mtulo wa munthu umtsegulira njira,numfikitsa pamaso pa akulu.","Woyamba kudzinenera ayang'anika wolungama;koma mnzake afika namuululitsa zake zonse.","Maere aletsa makangano,nulekanitsa amphamvu.","Kupembedza mbale utamchimwira nkovuta,kulanda mudzi wolimba nkosavuta;makangano akunga mipiringidzo ya linga.","Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m'kamwa mwake;iye nadzakhuta phindu la milomo yake.","Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo;wolikonda adzadya zipatso zake.","Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino;Yehova amkomera mtima.","Wosauka amadandaulira;koma wolemera ayankha mwaukali.","Woyanjana ndi ambiri angodziononga;koma lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira."]