bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.29 kB
JSON
["Nyenyeswa youma, pokhala mtendere,iposa nyumba yodzala nyama yansembe, pali makangano.","Kapolo wochita mwanzeruadzalamulira mwana wochititsa manyazi,nadzagawana nao abale cholowa.","Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng'anjo;koma Yehova ayesa mitima.","Wochimwa amasamalira milomo yolakwa;wonama amvera lilime losakaza.","Wochitira chiphwete aumphawi atonza Mlengi;wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka chilango.","Zidzukulu ndizo korona wa okalamba;ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.","Mlomo wangwiro suyenera chitsiru;ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.","Wolandira chokometsera mlandu achiyesa ngale;paliponse popita iye achenjera.","Wobisa cholakwa afunitsa chikondano;koma wobwerezabwereza mau afetsa ubwenzi.","Chidzudzulo chilowa m'kati mwa wozindikira,kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.","Woipa amafuna kupanduka kokha;koma adzamtumizira mthenga wankhanza.","Kukomana ndi chitsiru m'kupusa kwakekuopsa koposa chilombo chochichotsera anake.","Wobwezera zabwino zoipa,zoipa sizidzamchokera kwao.","Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi;tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.","Wokometsa mlandu wa wamphulupulu,ndi wotsutsa wolungama,onse awiriwa amnyansa Yehova.","Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la chitsiru,popeza wopusa alibe mtima?","Bwenzi limakonda nthawi zonse;ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.","Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina,napereka chikole pamaso pa mnzake.","Wokonda ndeu akonda kulakwa;ndipo wotalikitsa khomo lake afunafuna kuonongeka.","Wokhota mtima sadzapeza bwino;ndipo mwini lilime lokhota adzagwa m'zoipa.","Wobala chitsiru adzichititsa chisoni;ndipo atate wa wopusa sakondwa.","Mtima wosekerera uchiritsa bwino;koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.","Munthu woipa alandira chokometsera mlandu chotulutsa m'mfunga,kuti apatukitse mayendedwe a chiweruzo.","Nzeru ili pamaso pa wozindikira;koma maso a wopusa ali m'malekezero a dziko.","Mwana wopusa achititsa atate wake chisoni,namvetsa zowawa amake wombala.","Kulipiritsa wolungama sikuli kwabwino,ngakhale kukwapula akulu chifukwa aongoka mtima.","Wopanda chikamwakamwa apambana kudziwa;ndipo wofatsa mtima ali wanzeru.","Ngakhale chitsiru chikatonthola achiyesa chanzeru;posunama ali wochenjera."]