bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.62 kB
JSON
["Mkazi yense wanzeru amanga banja lake;koma wopusa alipasula ndi manja ake.","Woyenda moongoka mtima aopa Yehova;koma wokhota m'njira yake amnyoza.","M'kamwa mwa chitsiru muli nthyole ya kudzikuza;koma milomo ya anzeru idzawasunga.","Popanda zoweta modyera muti see;koma mphamvu ya ng'ombe ichulukitsa phindu.","Mboni yokhulupirika sidzanama;koma mboni yonyenga imalankhula zonama.","Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza;koma wozindikira saona vuto m'kuphunzira.","Pita pamaso pa munthu wopusa,sudzazindikira milomo yakudziwa.","Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake;koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.","Zitsiru zinyoza kupalamula;koma mwa oongoka mtima muli chiyanjano.","Mtima udziwa kuwawa kwakekwake;mlendo sadudukira ndi chimwemwe chake.","Nyumba ya oipa idzapasuka;koma hema wa oongoka mtima adzakula.","Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka;koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.","Ngakhale m'kuseka mtima uwawa;ndipo matsiriziro a chiphwete ndi chisoni.","Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira yake;koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.","Wachibwana akhulupirira mau onse;koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.","Wanzeru amaopa nasiya zoipa;koma wopusa amanyada osatekeseka.","Wokangaza kukwiya adzachita utsiru;ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.","Achibwana amalandira cholowa cha utsiru;koma ochenjera amavala nzeru ngati korona.","Oipa amagwadira abwino,ndi ochimwa pa makomo a olungama.","Waumphawi adedwa ndi anzake omwe;koma akukonda wolemera achuluka.","Wonyoza anzake achimwa;koma wochitira osauka chifundo adala.","Kodi oganizira zoipa sasochera?Koma akuganizira zabwino adzalandira chifundo ndi ntheradi.","M'ntchito zonse muli phindu;koma kulankhulalankhula kungopatsa umphawi.","Korona wa anzeru ndi chuma chao;utsiru wa opusa ndiwo utsiru.","Mboni yoona imalanditsa miyoyo;koma wolankhula zonama angonyenga.","Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.","Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,kupatutsa kumisampha ya imfa.","Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu;koma popanda anthu kalonga aonongeka.","Wosakwiya msanga apambana kumvetsa;koma wansontho akuza utsiru.","Mtima wabwino ndi moyo wa thupi;koma nsanje ivunditsa mafupa.","Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wake;koma wochitira wosauka chifundo amlemekeza.","Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake;koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.","Nzeru ikhalabe m'mtima wa wozindikira,nidziwika pakati pa opusa.","Chilungamo chikuza mtundu wa anthu;koma tchimo lichititsa fuko manyazi.","Mfumu ikomera mtima kapolo wochita mwanzeru;koma idzakwiyira wochititsa manyazi."]