bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.13 kB
JSON
["Wokonda mwambo akonda kudziwa;koma wakuda chidzudzulo apulukira.","Yehova akomera mtima munthu wabwino;koma munthu wa ziwembu amtsutsa.","Munthu sadzakhazikika ndi udyo,muzu wa olungama sudzasunthidwa.","Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake;koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.","Maganizo a olungama ndi chiweruzo;koma uphungu wa oipa unyenga.","Mau a oipa abisalira mwazi;koma m'kamwa mwa olungama muwalanditsa.","Oipa amagwa kuli zii;koma banja la olungama limaimabe.","Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yake;koma wokhota mtima adzanyozedwa.","Wonyozedwa, amene ali ndi kapolo,aposa wodzikuza, amene asowa zakudya.","Wolungama asamalira moyo wa choweta chake;koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.","Zakudya zikwanira wolima minda yake;koma wotsata anthu opanda pake asowa nzeru.","Woipa akhumba chokodwa ndi amphulupulu;koma muzu wa olungama umabala zipatso.","M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa;koma wolungama amatuluka m'mavuto.","Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake;zochita za manja ake zidzabwezedwa kwa iye.","Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake;koma wanzeru amamvera uphungu.","Mkwiyo wa chitsiru udziwika posachedwa;koma wanzeru amabisa manyazi.","Wolankhula ntheradi aonetsa chilungamo;koma mboni yonama imanyenga.","Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga;koma lilime la anzeru lilamitsa.","Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse;koma lilime lonama likhala kamphindi.","Chinyengo chili m'mitima ya oganizira zoipa;koma aphungu a mtendere amakondwa.","Palibe vuto lidzagwera wolungama;koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa.","Milomo yonama inyansa Yehova;koma ochita ntheradi amsekeretsa.","Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa;koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.","Dzanja la akhama lidzalamulira;koma waulesi adzakhala ngati kapolo.","Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu;koma mau abwino aukondweretsa.","Wolungama atsogolera mnzake;koma njira ya oipa iwasokeretsa.","Waulesi samaotcha nyama yake anaigwira;koma wolungama amalandira chuma chopambana cha anthu.","M'khwalala la chilungamo muli moyo;m'njira ya mayendedwe ake mulibe imfa."]