bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.37 kB
JSON
["Muyeso wonyenga unyansa Yehova;koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.","Pakudza kudzikuza padzanso manyazi;koma nzeru ili ndi odzichepetsa.","Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera;koma kukhota kwa achiwembu kudzawaononga.","Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo;koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.","Chilungamo cha wangwiro chimaongola njira yake;koma woipa adzagwa ndi zoipa zake.","Chilungamo cha oongoka mtima chidzawapulumutsa;koma achiwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.","Pomwalira woipa chidikiro chake chionongeka;chiyembekezo cha uchimo chionongeka.","Wolungama apulumuka kuvuto;woipa nalowa m'malo mwake.","Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake;koma olungama adzapulumuka pakudziwa.","Olungama akapeza bwino, mudzi usekera;nufuula pakuonongeka oipa.","Madalitso a olungama akuza mudzi;koma m'kamwa mwa oipa muupasula.","Wopeputsa mnzake asowa nzeru;koma wozindikira amatonthola.","Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi;koma wokhulupirika mtima abisa mau.","Popanda upo wanzeru anthu amagwa;koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.","Woperekera mlendo chikole adzaphwetekwapo;koma wakuda chikole akhala ndi mtendere.","Mkazi wodekha agwiritsa ulemu;aukali nagwiritsa chuma.","Wachifundo achitira moyo wake zokoma;koma wankhanza avuta nyama yake.","Woipa alandira malipiro onyenga;koma wofesa chilungamo aonadi mphotho.","Wolimbikira chilungamo alandira moyo;koma wolondola zoipa adzipha yekha.","Okhota mtima anyansa Yehova;koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.","Zoonadi, wochimwa sadzapulumuka chilango;koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa.","Monga chipini chagolide m'mphuno ya nkhumba,momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.","Chifuniro cha olungama chifikitsa zabwino zokha;koma chiyembekezo cha oipa mkwiyo.","Alipo wogawira, nangolemerabe;aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka.","Mtima wa mataya udzalemera;wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.","Womana tirigu anthu amtemberera;koma madalitso adzakhala pamtu pa wogulitsa.","Wopwaira ubwino afunitsa chikondwerero;koma zoipa zidzamfikira wozilondola.","Wokhulupirira chuma chake adzagwa;koma olungama adzaphuka ngati tsamba.","Wovuta banja lake adzalowa m'zomsautsa;wopusa adzatumikira wanzeru.","Chipatso cha wolungama ndi mtengo wa moyo;ndipo wokola mtima ali wanzeru.","Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno;koposa kotani woipa ndi wochimwa?"]