bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.44 kB
JSON
["Miyambo ya Solomoni:Mwana wanzeru akondweretsa atate;koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.","Chuma cha uchimo sichithangata;koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.","Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama;koma amainga chifuniro cha wochimwa.","Wochita ndi dzanja laulesi amasauka;koma dzanja la akhama lilemeretsa.","Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru;koma wogona pakutula ndi mwana wochititsa manyazi.","Madalitso ali pamtu pa wolungama;koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.","Amayesa wolungama wodala pomkumbukira;koma dzina la oipa lidzavunda.","Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo;koma chitsiru cholongolola chidzagwa.","Woyenda moongoka amayenda osatekeseka;koma wokhotetsa njira zake adzadziwika.","Wotsinzinira achititsa chisoni;koma wodzudzula momveka achita mtendere.","M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo;koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.","Udani upikisanitsa;koma chikondi chikwirira zolakwa zonse.","Nzeru ipezedwa m'milomo ya wozindikira;koma wopusa pamsana pake nthyole.","Anzeru akundika zomwe adziwa;koma m'kamwa mwa chitsiru muononga tsopano lino.","Chuma cha wolemera ndi mudzi wake wolimba;koma umphawi wao uononga osauka.","Ntchito za wolungama zipatsa moyo;koma phindu la oipa lichimwitsa.","Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo;koma wosiya chidzudzulo asochera.","Wobisa udani ali ndi milomo yonama;wonena ugogodi ndiye chitsiru.","Pochuluka mau zolakwa sizisoweka;koma wokhala chete achita mwanzeru.","Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika;koma mtima wa oipa uli wachabe.","Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri;koma zitsiru zimafa posowa nzeru.","Madalitso a Yehova alemeretsa,saonjezerapo chisoni.","Masewero a chitsiru ndiwo kuchita zoipa;koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.","Chomwe woipa achiopa chidzamfikira;koma chomwe olungama achifuna chidzapatsidwa.","Monga kavumbulu angopita, momwemo woipa kuli zii;koma olungama ndiwo maziko osatha.","Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso,momwemo waulesi kwa iwo amene amtuma.","Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku;koma zaka za oipa zidzafinimpha.","Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe;koma chidikiro cha oipa chidzaonongeka.","Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima;koma akuchita zoipa adzaonongeka.","Wolungama sadzachotsedwa konse;koma oipa sadzakhalabe m'dziko.","M'kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru;koma lilime lokhota lidzadulidwa.","Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa;koma m'kamwa mwa oipa munena zokhota."]