UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 3.86 kB
["Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.","Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOVA:","ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwika kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA.","Ndipo ndinakhazikitsanso nao chipangano changa, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo.","Ndamvanso kubuula kwa ana a Israele, amene Aejipito awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa.","Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo akulu;","ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aejipito.","Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova.","Ndipo Mose ananena chomwecho ndi ana a Israele; koma sanamvere Mose chifukwa cha kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera.","Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,","Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake.","Koma Mose ananena pamaso pa Yehova, ndi kuti, Onani, ana a Israele sanandimvere ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula?","Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israele, ndi za Farao mfumu ya Aejipito, kuti atulutse ana a Israele m'dziko la Ejipito.","Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana amuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amene ndiwo mabanja a Rubeni.","Ndi ana amuna a Simeoni ndiwo: Yemuwele, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo mwana wa mkazi wa Mkanani; amene ndiwo mabanja a Simeoni.","Ndipo maina a ana amuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.","Ana amuna a Geresoni ndiwo: Libini ndi Simei, mwa mabanja ao.","Ndi ana amuna a Kohati ndiwo: Amuramu ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu ndi kudza zitatu.","Ndipo ana amuna a Merari ndiwo: Mali ndi Musi. Amenewo ndiwo mabanja a Levi mwa kubadwa kwao.","Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.","Ndi ana amuna a Izihara ndiwo: Kora ndi Nefegi, ndi Zikiri.","Ndi ana amuna a Uziyele ndiwo: Misaele, ndi Elizafani, ndi Sitiri.","Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.","Ndipo ana amuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiyasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora.","Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao.","Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Tulutsani ana a Israele m'dziko la Ejipito mwa makamu ao.","Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aejipito, awatulutse ana a Israele m'Ejipito; Mose ndi Aroni amenewa.","Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m'dziko la Ejipito,","Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova; lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito zonsezi Ine ndizinena nawe.","Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndili wa milomo yosadula ndipo Farao adzandimvera bwanji?"]