bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 905 B
JSON
["Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere;Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.","Yehova ndiye wamkulu m'Ziyoni;ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.","Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa.Ili ndilo loyera.","Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo;Inu mukhazikitsa zolunjika,muchita chiweruzo ndi chilungamo m'Yakobo.","Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake:Iye ndiye Woyera.","Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni,ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake;anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.","Iye analankhula nao mu mtambo woti njo:Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.","Munawayankha, Yehova Mulungu wathu:munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira,mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao.","Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,ndipo gwadirani pa phiri lake loyera;pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera."]