UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.3 kB
["Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano;muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.","Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake;lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.","Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu;zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.","Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;ayenera amuope koposa milungu yonse.","Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano,koma Yehova analenga zakumwamba.","Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu.M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.","Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu,mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu.","Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake;bwerani nacho chopereka, ndipo fikani kumabwalo ake.","Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa,njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi.","Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu;dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke;adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.","Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi;nyanja ibume mwa kudzala kwake.","Munda ukondwerere ndi zonse zili m'mwemo;pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera.","Pamaso pa Yehova, pakuti akudza;pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansiAdzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo,ndi mitundu ya anthu ndi choonadi."]