bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.81 kB
JSON
["Mulungu wakubwezera chilango,Yehova, Mulungu wakubwezera chilango, muoneke wowala.","Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi:Bwezerani odzikuza choyenera iwo.","Oipa adzatumpha ndi chimwemwe kufikira liti, Yehova?Oipa adzatero kufikira liti?","Anena mau, alankhula zowawa;adzitamandira onse ochita zopanda pake.","Aphwanya anthu anu, Yehova,nazunza cholandira chanu.","Amapha wamasiye ndi mlendo,nawapha ana amasiye.","Ndipo amati, Yehova sachipenya,ndi Mulungu wa Yakobo sachisamalira.","Zindikirani, opulukira inu mwa anthu;ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?","Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva?Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya?","Kodi Iye wakulangiza mitundu ya anthu, ndiye wosadzudzula?Si ndiye amene aphunzitsa munthu nzeru?","Yehova adziwa zolingalira za munthu,kuti zili zachabe.","Wodala munthu amene mumlanga, Yehova;ndi kumphunzitsa m'chilamulo chanu;","kuti mumpumitse masiku oipa;kufikira atakumbira woipa mbuna.","Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake,ndipo sadzataya cholandira chake.","Pakuti chiweruzo chidzabwera kunka kuchilungamo,ndipo oongoka mtima onse adzachitsata.","Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa?Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?","Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova,moyo wanga ukadakhala kuli chete.","Pamene ndinati, Litereka phazi langa,chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza.","Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga,zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.","Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza,wakupanga chovuta chikhale lamulo?","Asonkhana pamodzi pa moyo wa wolungama,namtsutsa wa mwazi wosachimwa.","Koma Yehova wakhala msanje wanga;ndi Mulungu wanga thanthwe lothawirapo ine.","Ndipo anawabwezera zopanda pake zao,nadzawaononga m'choipa chao;Yehova Mulungu wathu adzawaononga."]