UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.3 kB
["Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwambaadzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.","Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa;Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.","Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi,kumliri wosakaza.","Adzakufungatira ndi nthenga zake,ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake;choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.","Sudzaopa choopsa cha usiku,kapena muvi wopita usana;","kapena mliri woyenda mumdima,kapena chionongeko chakuthera usana.","Pambali pako padzagwa chikwi,ndi zikwi khumi pa dzanja lamanja lako;sichidzakuyandikiza iwe.","Koma udzapenya ndi maso ako,nudzaona kubwezera chilango oipa.","Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga!Udaika Wam'mwambamwamba chokhalamo chako;","palibe choipa chidzakugwera,ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako.","Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe,akusunge m'njira zako zonse.","Adzakunyamula pa manja ao,ungagunde phazi lako pamwala.","Udzaponda mkango ndi mphiri;udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.","Popeza andikondadi ndidzampulumutsa;ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.","Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha;kunsautso ndidzakhala naye pamodzi;ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.","Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri,ndi kumuonetsera chipulumutso changa."]