UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.5 kB
["Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa,ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.","Pemphero langa lidze pamaso panu;munditcherere khutu kukuwa kwanga.","Pakuti mzimu wanga wadzala nao mavuto,ndi moyo wanga wayandikira kumanda.","Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje;ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu.","Wotayika pakati pa akufa,ngati ophedwa akugona m'manda,amene simuwakumbukiranso;ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.","Munandiika kunsi kwa dzenje,kuli mdima, kozama.","Mkwiyo wanu utsamira pa ine,ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.","Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali;munandiika ndiwakhalire chonyansa.Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.","Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga:Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse;nditambalitsira manja anga kwa Inu.","Kodi mudzachitira akufa zodabwitsa?Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani?","Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi,chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko?","Zodabwitsa zanu zidadziwika mumdima kodi,ndi chilungamo chanu m'dziko la chiiwaliko?","Koma ndinafuulira kwa Inu, Yehova,ndipo pemphero langa lifika kwa Inu mamawa.","Yehova mutayiranji moyo wanga?Ndi kundibisira nkhope yanu?","Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga;posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.","Kuzaza kwanu kwandimiza;zoopsa zanu zinandiononga.","Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse;zinandizinga pamodzi.","Munandichotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa,odziwana nane akhala kumdima."]