UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.19 kB
["Pokhala Inu mpotikonda ndithu,Yehova wa makamu!","Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova;mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.","Mbawanso inapeza nyumba,ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake,pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu,mfumu yanga ndi Mulungu wanga.","Odala iwo akugonera m'nyumba mwanu;akulemekezani chilemekezere.","Wodala munthu amene mphamvu yake ili mwa Inu;mumtima mwake muli makwalala a ku Ziyoni.","Popyola chigwa cha kulira misozi achiyesa cha akasupe;inde mvula ya chizimalupsa ichidzaza ndi madalitso.","Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu,aoneka pamaso pa Mulungu m'Ziyoni.","Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa.Tcherani khutu, Mulungu wa Yakobo.","Onani, Mulungu, ndinu chikopa chathu;ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.","Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likomakoposa masiku ambirimbiri akukhala pena.Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga,kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.","Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa;Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero;sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.","Yehova wa makamu,wodala munthu wakukhulupirira Inu."]