UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.28 kB
["Mulungu musakhale chete;musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu.","Pakuti taonani, adani anu aphokosera,ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu.","Apangana mochenjerera pa anthu anu,nakhalira upo pa obisika anu.","Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu;ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.","Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi;anachita chipangano cha pa Inu.","Mahema a Edomu ndi a Aismaele;Mowabu ndi Ahagiri;","Gebala ndi Amoni ndi Amaleke;Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala m'Tiro.","Asiriya anaphatikana nao;anakhala dzanja la ana a Loti.","Muwachitire monga munachitira Midiyani;ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni,","amene anaonongeka ku Endori;anakhala ngati ndowe ya kumunda.","Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu;mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna,","amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu.","Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu;ngati ziputu zomka ndi mphepo.","Monga moto upsereza nkhalango,ndi monga lawi liyatsa mapiri.","Momwemo muwatsate ndi namondwe,nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu.","Achititseni manyazi pankhope pao;kuti afune dzina lanu, Yehova.","Achite manyazi, naopsedwe kosatha;ndipo asokonezeke, naonongeke.","Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova,ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi."]