UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 819 B
["Yehova, Ambuye wathu,dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.","M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu,chifukwa cha otsutsana ndi Inu,kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.","Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu,mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,","munthu ndani kuti mumkumbukira?Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?","Pakuti munamchepsa pang'ono ndi Mulungu,munamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.","Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu;mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake;","nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo,ndi nyama za kuthengo zomwe;","mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja.Zopita m'njira za m'nyanja.","Yehova, Ambuye wathu,dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!"]