bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.36 kB
JSON
["Mulungu, akunja alowa m'cholandira chanu;anaipsa Kachisi wanu woyera;anachititsa Yerusalemu bwinja.","Anapereka mitembo ya atumiki anu ikhalechakudya cha mbalame za mlengalenga,nyama ya okondedwa anu anaipereka kwa zilombo za m'dziko.","Anakhetsa mwazi wao ngati madzi pozungulira Yerusalemu;ndipo panalibe wakuwaika.","Takhala chotonza cha anansi athu,ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.","Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti?Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?","Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziwa Inu,ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu.","Pakuti anathera Yakobo,napasula pokhalira iye.","Musakumbukire motitsutsa mphulupulu za makolo athu;nsoni zokoma zanu zitipeze msanga,pakuti tafooka kwambiri.","Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu,chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu;ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu,chifukwa cha dzina lanu.","Anenerenji amitundu, Ali kuti Mulungu wao?Kubwezera chilango cha mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsakudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu.","Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu;monga mwa mphamvu yanu yaikulu lolani ana a imfa atsale.","Ndipo anansi athu amene anatonza Inumuwabwezere chotonza chao,kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.","Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panutidzakuyamikani kosatha;tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo."]