UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.86 kB
["Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu,ndi mwana wa mfumu chilungamo chanu.","Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m'chilungamo,ndi ozunzika anu ndi m'chiweruzo.","Mapiri adzatengera anthu mtendere,timapiri tomwe, m'chilungamo.","Adzaweruza ozunzika a mwa anthu,adzapulumutsa ana aumphawi,nadzaphwanya wosautsa.","Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi,kufikira mibadwomibadwo.","Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga,monga mvula yothirira dziko.","Masiku ake wolungama adzakhazikika;ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.","Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja,ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.","Okhala m'chipululu adzagwadira pamaso pake;ndi adani ake adzaluma nthaka.","Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka;mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.","Inde mafumu onse adzamgwadira iye,amitundu onse adzamtumikira.","Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo;ndi wozunzika amene alibe mthandizi.","Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi,nadzapulumutsa moyo wa aumphawi.","Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa;ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake.","Ndipo iye adzakhala ndi moyo;ndipo adzampatsa golide wa ku Sheba;nadzampempherera kosalekeza;adzamlemekeza tsiku lonse.","M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochulukapamwamba pa mapiri;zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni,ndipo iwo a m'mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.","Dzina lake lidzakhala kosatha,momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu.Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye;amitundu onse adzamutcha wodala.","Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele,amene achita zodabwitsa yekhayo.","Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha;ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake.Amen, ndi Amen.","Mapemphero a Davide mwana wa Yese atha."]