bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 3.57 kB
JSON
["Auke Mulungu, abalalike adani ake;iwonso akumuda athawe pamaso pake.","Muwachotse monga utsi uchotseka;monga phula lisungunuka pamoto,aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.","Koma olungama akondwere;atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu;ndipo asekere nacho chikondwerero.","Imbirani Yehova, liimbireni nyimbo dzina lake;undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha;dzina lake ndiye Yehova;ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.","Mulungu, mokhala mwake moyera,ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.","Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha;atulutsa am'ndende alemerere;koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.","Pakutuluka paja, Inu Mulungu, ndi kutsogolera anthu anu,pakuyenda paja Inu m'chipululu.","Dziko lapansi linagwedezeka,inde thambo linakha pamaso pa Mulungu;Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu,Mulungu wa Israele.","Inu, Mulungu, munavumbitsa chimvula,munatsitsimutsa cholowa chanu pamene chidathodwa.","Gulu lanu linakhala m'dziko muja.Mwa ukoma wanu munalikonzera ozunzika, Mulungu.","Ambuye anapatsa mau,akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.","Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa,ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.","Pogona inu m'makola a zoweta,mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva,ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.","Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m'dzikomo,munayera ngati matalala m'Zalimoni.","Phiri la Basani ndilo phiri la Mulungu;Phiri la Basani ndilo phiri la mitumitu.","Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu,ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko?Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.","Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri,inde zikwi zowirikizawirikiza,Ambuye ali pakati pao, monga m'Sinai, m'malo opatulika.","Munakwera kunka kumwamba,munapita nao undende kuuyesa ndende;munalandira zaufulu mwa anthu,ngakhale mwa opikisana nanu,kuti Yehova Mulungu akakhale nao.","Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu,ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.","Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso;ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa.","Indedi Mulungu adzaphwanya mutu wa adani ake,pakati pa mutu pa iye woyendabe m'kutsutsika kwake.","Ambuye anati, Ndidzawatenganso ku Basani,ndidzawatenganso kozama kwa nyanja,","kuti uviike phazi lako m'mwazi,kuti malilime a agalu ako alaweko adani ako.","Anapenya mayendedwe anu, Mulungu,mayendedwe a Mulungu wanga, mfumu yanga, m'malo oyera.","Oimbira anatsogolera, oimba zoimba anatsata m'mbuyo,pakatipo anamwali oimba mangaka.","Lemekezani Mulungu m'masonkhano,ndiye Ambuye, inu a gwero la Israele.","Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwachita ufumu,akulu a Yuda, ndi a upo wao,akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.","Mulungu wako analamulira mphamvu yako,Limbitsani, Mulungu, chimene munatichitira.","Chifukwa cha Kachisi wanu wa m'Yerusalemumafumu adzabwera nacho chaufulu kukupatsani.","Dzudzulani chilombo cha m'bango,khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu,yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva;anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.","Akulu adzafumira ku Ejipito;Kusi adzafulumira kutambalitsa manja ake kwa Mulungu.","Imbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu;imbirani Ambuye zomlemekeza.","Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba,oyambira kale lomwe;taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu.","Vomerezani kuti mphamvu nja Mulungu;ukulu wake uli pa Israele,ndi mphamvu yake m'mitambo.","Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu;Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu akemphamvu ndi chilimbiko.Alemekezeke Mulungu."]