bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.3 kB
JSON
["M'Ziyoni akulemekezani Inu mwachete, Mulungu,adzakuchitirani Inu chowindachi.","Wakumva pemphero Inu,zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.","Mphulupulu zinandilaka;koma mudzafafaniza zolakwa zathu.","Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa,akhale m'mabwalo anu.Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu,za m'malo oyera a Kachisi wanu.","Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo,Mulungu wa chipulumutso chathu;ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi,ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.","Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu;pozingidwa nacho chilimbiko.","Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja,kukuntha kwa mafunde ake,ndi phokoso la mitundu ya anthu.","Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzachita manthachifukwa cha zizindikiro zanu;mukondweretsa apo patulukira dzuwa, ndi apo lilowera.","Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira,mulilemeza kwambiri;mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi,muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.","Mukhutitsa nthaka yake yolima;mufafaniza nthumbira zake;muiolowetsa ndi mvumbi;mudalitsa mmera wake.","Muveka chakachi ndi ukoma wanu;ndipo mabande anu akukha zakucha.","Akukha pa mabusa a m'chipululu;ndipo mapiri azingika nacho chimwemwe.","Podyetsa mpodzaza ndi zoweta;ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu;zifuula mokondwera, inde ziimbira."]