UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 852 B
["Imvani Yehova, mau anga, m'kudandaula kwanga;sungani moyo wanga angandiopse mdani.","Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa;pa phokoso la ochita zopanda pake.","Amene anola lilime lao ngati lupanga,napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;","kuponyera wangwiro mobisika:Amponyera modzidzimutsa, osaopa.","Alimbikitsana m'chinthu choipa;apangana za kutchera misampha mobisika;akuti, Adzaiona ndani?","Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha;chingakhale cha m'kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama.","Koma Mulungu adzawaponyera muvi;adzalaswa modzidzimutsa.","Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa;onse akuwaona adzawathawa.","Ndipo anthu onse adzachita mantha;nadzabukitsa chochita Mulungu,nadzasamalira ntchito yake.","Wolungama adzakondwera mwa Yehova,nadzakhulupirira Iye;ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza."]