bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.04 kB
JSON
["Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga;ndidzakufunani m'matanda kucha.Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu,thupi langa lilirira Inu,m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.","Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu,monga ndinakuonani m'malo oyera.","Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake;milomo yanga idzakulemekezani.","Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga;ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.","Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi chonona;ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezanindi milomo yakufuula mokondwera.","Pokumbukira Inu pa kama wanga,ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.","Pakuti munakhala mthandizi wanga;ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.","Moyo wanga uumirira Inu.Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.","Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,adzalowa m'munsi mwake mwa dziko.","Adzawapereka kumphamvu ya lupanga;iwo adzakhala gawo la ankhandwe.","Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;yense wakulumbirira iye adzatamandira;pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa."]