bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 897 B
JSON
["Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama?Muweruza ana anthu molunjika kodi?","Inde, mumtima muchita zosalungama;pa dziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu.","Oipa achita chilendo chibadwire,asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza.","Ululu wao ukunga wa njoka;akunga mphiri yogontha m'khutu, itseka m'khutu mwake.","Imene siimvera liu la oitana,akuchita matsenga mochenjeratu.","Thyolani mano ao m'kamwa mwao, Mulungu,zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.","Apitetu ngati madzi oyenda;popiringidza mivi yake ikhale yodukaduka.","Apite ngati nkhono yosungunuka;asaone dzuwa monga mtayo.","Miphika yanu isanagwire moto waminga,adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.","Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango,adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa.","Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama.Indedi, pali Mulungu wakuweruza pa dziko lapansi."]