UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 865 B
["Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe?Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse.","Lilime lako likupanga zoipa;likunga lumo lakuthwa, lakuchita monyenga.","Ukonda choipa koposa chokoma;ndi bodza koposa kunena chilungamo,","ukonda mau onse akuononga,lilime lachinyengo, iwe.","Potero Mulungu adzakupasula kunthawi zonse,adzakuchotsa nadzakukwatula m'hema mwako,nadzakuzula, kukuchotsa m'dziko la amoyo.","Ndipo olungama adzachiona, nadzaopa,nadzamseka, ndi kuti,","Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake;amene anatama kuchuluka kwa chuma chake,nadzilimbitsa m'kuipsa kwake.","Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi wa azitonam'nyumba ya Mulungu.Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi.","Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munachichita ichi,ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ichi nchokoma,pamaso pa okondedwa anu."]