bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.83 kB
JSON
["Mundichitire ine chifundo, Mulungu,monga mwa kukoma mtima kwanu;monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanumufafanize machimo anga.","Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga,ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.","Chifukwa ndazindikira machimo anga;ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire.","Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa,ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu;kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu,mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.","Onani, ndinabadwa m'mphulupulu,ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.","Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo;ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.","Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera;munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala.","Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera,kuti mafupawo munawathyola akondwere.","Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga,ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.","Mundilengere mtima woyera, Mulungu;mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.","Musanditaye kundichotsa pamaso panu;musandichotsere Mzimu wanu Woyera.","Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu;ndipo mzimu wakulola undigwirizize.","Pomwepo ndidzalangiza ochimwa njira zanu;ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.","Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu,ndinu Mulungu wa chipulumutso changa;lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.","Ambuye, tsegulani pa milomo yanga;ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.","Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka;nsembe yopsereza simuikonda.","Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka;Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.","Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu;mumange malinga a miyala a Yerusalemu.","Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo,ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu;pamenepo adzaperekang'ombe pa guwa lanu la nsembe."]