UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.22 kB
["Mverani mau anga, Yehova, Zindikirani kulingirira kwanga.","Tamvetsani mau a kufuula kwanga,Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga;pakuti kwa Inu ndimapemphera.","M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga;m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.","Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipamphulupulu siikhala ndi Inu.","Opusa sadzakhazikika pamaso panu,mudana nao onse akuchita zopanda pake.","Mudzaononga iwo akunena bodza;munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo,Yehova anyansidwa naye.","Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanundidzalowa m'nyumba yanu;ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.","Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu,chifukwa cha akundizondawo;mulungamitse njira yanu pamaso panga.","Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika;m'kati mwao m'mosakaza;m'mero mwao ndi manda apululu;lilime lao asyasyalika nalo.","Muwayese otsutsika Mulungu;agwe nao uphungu wao.M'kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse;pakuti anapikisana ndi Inu.","Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu,afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira;nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.","Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo;mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa."]