UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.69 kB
["Dzamveni kuno, anthu inu nonse;tcherani khutu, inu nonse amakono,","awamba ndi omveka omwe,achuma ndi aumphawi omwe.","Pakamwa panga padzanena zanzeru;ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziwitso.","Ndidzatchera khutu kufanizo,ndidzafotokozera chophiphiritsa changa poimbira.","Ndidzaoperanji masiku oipa,pondizinga amphulupulu onditsata kuchidendene?","Iwo akutama kulemera kwao;nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao;","kuombola mbale sangadzamuombole,kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.","Popeza chiombolo cha moyo wao ncha mtengo wake wapatali,ndipo chilekeke nthawi zonse.","Kuti akhale ndi moyo osafa,osaona chivundi.","Pakuti aona anzeru amafa,monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo,nasiyira ena chuma chao.","Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire,ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo;atchapo dzina lao padziko pao.","Koma munthu wa ulemu wake sakhalitsa,afanana ndi nyama za kuthengo, afanana nazo.","Njira yao yino ndiyo kupusa kwao,koma akudza m'mbuyo avomereza mau ao.","Aikidwa m'manda ngati nkhosa;mbusa wao ndi imfa.Ndipo m'mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao;ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda,kuti pokhala pake padzasowa.","Koma Mulungu adzaombola moyo wangakumphamvu ya manda.Pakuti adzandilandira ine.","Usaope polemezedwa munthu,pochuluka ulemu wa nyumba yake;","pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse;ulemu wake sutsika naye kumtsata m'mbuyo.","Angakhale anadalitsa moyo wake pokhala ndi moyo,ndipo anthu akulemekeza iwe, podzichitira wekha zokoma.","Adzamuka kumbadwo wa makolo ake;sadzaona kuunika nthawi zonse.","Munthu waulemu, koma wosadziwitsa,afanana ndi nyama za kuthengo, afanana nazo."]