UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.18 kB
["Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi,m'mudzi wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.","Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokomakumbali zake za kumpoto,ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi,mudzi wa mfumu yaikulu.","Mulungu adziwika m'zinyumba zake ngati msanje.","Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana,anapitira pamodzi.","Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa;anaopsedwa, nathawako.","Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira;anamva chowawa, ngati wam'chikuta.","Muswa zombo za ku Tarisisi ndi mphepo ya kum'mawa.","Monga tidamva, momwemo tidapenyam'mudzi wa Yehova wa makamu, m'mudzi wa Mulungu wathu,Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.","Tidalingalira zachifundo chanu, Mulungu,m'kati mwa Kachisi wanu.","Monga dzina lanu, Mulungu,momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi;m'dzanja lamanja lanu mudzala chilungamo.","Likondwere phiri la Ziyoni,asekere ana akazi a Yuda,chifukwa cha maweruzo anu.","Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge,werengani nsanja zake.","Penyetsetsani malinga ake,yesetsani zinyumba zake;kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo.","Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathukunthawi za nthawi,adzatitsogolera kufikira imfa."]