UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 994 B
["Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu,thandizo lopezekeratu m'masautso.","Chifukwa chake sitidzachita mantha,lingakhale lisandulika dziko lapansi,angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.","Chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu,nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake.","Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mudzi wa Mulungu.Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.","Mulungu ali m'kati mwake, sudzasunthika,Mulungu adzauthandiza mbandakucha.","Amitundu anapokosera, maufumu anagwedezeka,ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.","Yehova wa makamu ali ndi ife;Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.","Idzani, penyani ntchito za Yehova,amene achita zopululutsa pa dziko lapansi.","Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;athyola uta, nadula nthungo;atentha magaleta ndi moto.","Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu,Ndidzabuka mwa amitundu,ndidzabuka pa dziko lapansi.","Yehova wa makamu ali ndi ife,Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu."]