UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 679 B
["Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo.Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.","Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji?Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?","Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere;zindifikitse kuphiri lanu loyera,kumene mukhala Inuko.","Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu,kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni,ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.","Udziweramiranji moyo wanga iwe?Ndi kuzingwa m'kati mwanga?Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso,ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga."]