UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.47 kB
["Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje;motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.","Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu,la kwa Mulungu wamoyo.Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?","Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa,usana ndi usiku;pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse,Mulungu wako ali kuti?","Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine,pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu,ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu,ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika,ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.","Udziweramiranji moyo wanga iwe?Ndi kuzingwa m'kati mwanga?Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikansochifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.","Mulungu wanga, moyo wangaudziweramira m'kati mwanga;chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani,ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.","Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya,pa mkokomo wa matiti anu;mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.","Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake,ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine.Inde pemphero la kwa Yehova wa moyo wanga.","Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa,mwandiiwala chifukwa ninji?Ndimayenderanji wakulirachifukwa cha kundipsinja mdaniyo?","Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga;pakunena ndine dzuwa lonse,Mulungu wako ali kuti?","Udziweramiranji moyo wanga iwe?Ndi kuzingwa m'kati mwanga?Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso,ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga."]