bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.19 kB
JSON
["Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake;wokwiriridwa choipa chake.","Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zake;ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo.","Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalambandi kubuula kwanga tsiku lonse.","Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine;uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.","Ndinavomera choipa changa kwa Inu;ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa.Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga;ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.","Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu,pa nthawi ya kupeza Inu;indetu pakusefuka madzi aakulusadzamfikira iye.","Inu ndinu mobisalira mwanga;m'nsautso mudzandisunga;mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.","Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo;ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.","Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru;zomangira zao ndizo cham'kamwa ndi chapamutu zakuwakokera,pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.","Zisoni zambiri zigwera woipa;koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.","Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima;ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima."]