UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.08 kB
["Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa,ndipo simunandikondwetsera adani anga.","Yehova, Mulungu wanga,ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa.","Yehova munabweza moyo wanga kumanda,munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje.","Imbirani Yehova, inu okondedwa ake,ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.","Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha;koma kuyanja kwake moyo wonse.Kulira kuchezera,koma mamawa kuli kufuula kokondwera.","Ndipo ine, ndinanena m'phindu langa,sindidzagwedezeka nthawi zonse.","Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu;munabisa nkhope yanu; ndinaopa.","Ndinafuulira kwa Inu, Yehova;kwa Yehova ndinapemba,","M'mwazi mwanga muli phindu lanji,potsikira ine kudzenje?Ngati fumbi lidzayamika Inu?Ngati lidzalalikira choonadi chanu?","Mverani, Yehova, ndipo ndichitireni chifundo,Yehova, mundithandize ndi Inu.","Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera;munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero,","kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete.Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse."]