UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.7 kB
["Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa;ndidzaopa yani?Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga;ndidzachita mantha ndi yani?","Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga,inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.","Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole,mtima wanga sungachite mantha;ingakhale nkhondo ikandiukira,inde pomweponso ndidzakhulupirira.","Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova,ndidzachilondola ichi,Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,kupenya kukongola kwake kwa Yehovandi kufunsitsa m'Kachisi wake.","Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake,adzandibisa m'tsenjezi mwa chihema chake;pathanthwe adzandikweza.","Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezekapamwamba pa adani anga akundizinga;ndipo ndidzapereka m'chihema mwakensembe za kufuula mokondwera;ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.","Imvani, Yehova, liu langa pofuula ine;mundichitirenso chifundo ndipo mundivomereze.","Pamene munati, Funani nkhope yanga;mtima wanga unati kwa Inu.Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.","Musandibisire ine nkhope yanu;musachotse kapolo wanu ndi kukwiya.Inu munakhala thandizo langa;musanditaye, ndipo musandisiyeMulungu wa chipulumutso changa.","Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga,koma Yehova anditola.","Mundiphunzitse njira yanu, Yehova,munditsogolere pa njira yachidikha,chifukwa cha adani anga.","Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa,chifukwa zinandiukira mboni zonamandi iwo akupumira zachiwawa.","Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehovam'dziko la amoyo, ndikadatani!","Yembekeza Yehova,limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako;inde, yembekeza Yehova."]