UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.8 kB
["Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa,ndi kwa mau a kubuula kwanga?","Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza;ndipo usiku, sindikhala chete.","Koma Inu ndinu woyera,wakukhala m'malemekezo a Israele.","Makolo athu anakhulupirira Inu;anakhulupirira, ndipo munawalanditsa.","Anafuula kwa Inu, napulumutsidwa;anakhulupirira Inu, ndipo sanachite manyazi.","Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai,chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.","Onse akundipenya andiseka;akwenzula, apukusa mutu, nati,","Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa,amlanditse tsopano popeza akondwera naye.","Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa;wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga.","Chibadwire ine anandisiyira Inu,kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu.","Musandikhalire kutali; pakuti nsautso ili pafupi,pakuti palibe mthandizi.","Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga;mphongo zolimba za ku Basani zandizungulira.","Andiyasamira m'kamwa mwao,ngati mkango wozomola ndi wobangula.","Ndathiridwa pansi monga madzi,ndipo mafupa anga onse anaguluka.Mtima wanga ukunga sera;wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.","Mphamvu yanga yauma ngati phale;ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga;ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.","Pakuti andizinga agalu,msonkhano wa oipa wanditsekereza;andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.","Ndikhoza kuwerenga mafupa anga onse;iwo ayang'ana nandipenyetsetsa ine.","Agawana zovala zanga,nachita maere pa malaya anga.","Koma Inu, Yehova, musakhale kutali;mphamvu yanga Inu, mufulumire kundithandiza.","Landitsani moyo wanga kulupanga;wokondedwa wanga kumphamvu ya galu,","ndipulumutseni m'kamwa mwa mkango;inde mwandiyankha ine ndili pa nyanga za njati.","Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga,pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.","Inu akuopa Yehova, mumlemekeze;inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu;ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele.","Pakuti sanapeputsa ndipo sananyansidwendi zunzo la wozunzika;ndipo sanambisire nkhope yake;koma pomfuulira Iye, anamva.","Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu,zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.","Ozunzika adzadya nadzakhuta,adzayamika Yehova iwo amene amfuna,ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.","Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukiranadzatembenukira kwa Yehova,ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.","Pakuti ufumuwo ngwa Yehova;Iye achita ufumu mwa amitundu.","Onenepa onse a pa dziko lapansi adzadya nadzagwadira;onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake,ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.","Mbumba ya anthu idzamtumikira;kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza.","Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chakekwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita."]