UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.12 kB
["Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu;adzakondwera kwakukulu m'chipulumutso chanu!","Mwampatsa iye chikhumbo cha mtima wake,ndipo simunakana pempho la milomo yake.","Pakuti mufika kwa iye ndi madalitso okoma;muika korona wa golide woyengetsa pamutu pake.","Anakupemphani moyo, mwampatsa iye;mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi.","Ulemerero wake ngwaukulu mwa chipulumutso chanu;mumchitira iye ulemu ndi ukulu.","Pakuti mumuikira madalitso kunthawi zonse;mumkondweretsa ndi chimwemwe pankhope panu.","Pakuti mfumu akhulupirira Yehova,ndipo mwa chifundo cha Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye.","Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse,dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu.","Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu.Yehova adzawatha m'kukwiya kwake,ndipo moto udzawanyeketsa.","Mudzaziononga zobala zao kuzichotsa pa dziko lapansi,ndi mbeu zao mwa ana a anthu.","Pakuti anakupangirani choipa,anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita.","Pakuti mudzawabweza m'mbuyo,popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao.","Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu;potero tidzaimba ndi kulemekeza chilimbiko chanu."]