bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.41 kB
JSON
["Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu;ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.","Usana ndi usana uchulukitsa mau,ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.","Palibe chilankhulidwe, palibe mau;liu lao silimveka.","Muyeso wao wapitirira pa dziko lonse lapansi,ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu.Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,","ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m'chipinda mwake,likondwera ngati chiphona kuthamanga m'njira.","Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo,ndipo kuzungulira kwake lifikira ku malekezero ake;ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake.","Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo;mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.","Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima;malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.","Kuopa Yehova kuli mbee, kwakukhalabe nthawi zonse;maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse.","Ndizo zifunika koposa golide,inde, golide wambiri woyengetsa;zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.","Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo,m'kuzisunga izo muli mphotho yaikulu.","Adziwitsa zolowereza zake ndani?Mundimasule kwa zolakwa zobisika.","Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama;zisachite ufumu pa ine.Pamenepo ndidzakhala wangwiro,ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.","Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wangaavomerezeke pamaso panu,Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga."]