bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.03 kB
JSON
["Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.","Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga,ndilibe chabwino china choposa Inu.","Za oyera mtima okhala pa dziko lapansi,iwo ndiwo omveka mbiri,mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.","Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina.Sindidzathira nsembe zao zamwazi,ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga.","Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa,ndinu wondigwirira cholandira changa.","Zingwe zandigwera mondikondweretsa;inde chosiyira chokoma ndili nacho.","Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu,usikunso impso zanga zindilangiza.","Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse;popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.","Chifukwa chake wasekera mtima wanga,nukondwera ulemu wanga;mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.","Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda;simudzalola wokondedwa wanu avunde.","Mudzandidziwitsa njira ya moyo,pankhope panu pali chimwemwe chokwanira;m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya."]