UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.1 kB
["Aleluya.Lemekezani Yehova kochokera kumwamba;mlemekezeni m'misanje.","Mlemekezeni, angelo ake onse;mlemekezeni, makamu ake onse.","Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi;mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira.","Mlemekezeni, m'mwambamwamba,ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.","Alemekeze dzina la Yehova;popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.","Anazikhazikanso kunthawi za nthawi;anazipatsa chilamulo chosatumphika.","Lemekezani Yehova kochokera ku dziko lapansi,zinsomba inu, ndi malo ozama onse;","moto ndi matalala, chipale chofewa ndi nkhungu;mphepo ya namondwe, yakuchita mau ake;","mapiri ndi zitunda zonse;mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse:","Nyama za kuthengo ndi zoweta zonse;zokwawa, ndi mbalame zakuuluka.","Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu;zinduna ndi oweruza onse a padziko.","Anyamata ndiponso anamwali;okalamba pamodzi ndi ana.","Alemekeze dzina la Yehova;pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka;ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.","Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake,chilemekezo cha okondedwa ake onse;ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye.Aleluya."]