bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.42 kB
JSON
["Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma;pakuti chikondwetsa ichi, chilemekezo chiyenera.","Yehova amanga Yerusalemu;asokolotsa otayika a Israele.","Achiritsa osweka mtima,namanga mabala ao.","Awerenga nyenyezi momwe zili;azitcha maina zonsezi.","Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri;nzeru yake njosatha.","Yehova agwiriziza ofatsa;atsitsira oipa pansi.","Yamikani Yehova ndi kuthira mang'ombe;muimbireni Mulungu wathu zomlemekeza pazeze:","Amene aphimba thambo ndi mitambo,amene akonzera mvula nthaka,amene aphukitsa msipu pamapiri.","Amene apatsa zoweta chakudya chao,ana a khungubwi alikulira.","Mphamvu ya kavalo siimkonda:Sakondwera nayo miyendo ya munthu.","Yehova akondwera nao akumuopa Iye,iwo akuyembekeza chifundo chake.","Yerusalemu, lemekezani Yehova;Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu.","Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu:Anadalitsa ana anu m'kati mwanu.","Ndiye amene akhalitsa malire anu mumtendere;akukhutitsani ndi tirigu wakucha bwino.","Atumiza lamulo lake kudziko lapansi;mau ake athamanga liwiro.","Apatsa chipale chofewa ngati ubweya;awaza chisanu ngati phulusa.","Aponya matalala ake ngati zidutsu:Adzaima ndani pa kuzizira kwake?","Atumiza mau ake nazisungunula;aombetsa mphepo yake, ayenda madzi ake.","Aonetsa mau ake kwa Yakobo;malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele.","Sanatero nao anthu a mtundu wina;ndipo za maweruzo ake, sanawadziwe.Aleluya."]