UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 908 B
["Aleluya;Ulemekeze Yehova, moyo wanga.","Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga;ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.","Musamakhulupirira zinduna,kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.","Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake;tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.","Wodala munthu amene akhala nayeMulungu wa Yakobo kuti amthandize,chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.","Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi,nyanja ndi zonse zili m'mwemo.Ndiye wakusunga choonadi kosatha,","ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika;ndiye wakupatsa anjala chakudya;Yehova amasula akaidi.","Yehova apenyetsa osaona;Yehova aongoletsa onse owerama;Yehova akonda olungama.","Yehova asunga alendo;agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye;koma akhotetsa njira ya oipa.","Yehova adzachita ufumu kosatha,Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo.Aleluya."]