bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.55 kB
JSON
["Wolemekezeka Yehova thanthwe langa,wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo,zala zanga zigwirane nao:","Ndiye chifundo changa, ndi linga langa,msanje wanga, ndi Mpulumutsi wanga;chikopa changa, ndi Iye amene ndimtama;amene andigonjetsera anthu anga.","Yehova, munthu ndani kuti mumdziwa?Mwana wa munthu kuti mumsamalira?","Munthu akunga mpweya;masiku ake akunga mthunzi wopitirira.","Weramutsani thambo lanu, Yehova, nimutsike:Khudzani mapiri ndipo adzafuka.","Ng'animitsani mphezi, ndi kuwabalalitsa;tumizani mivi yanu, ndi kuwapirikitsa.","Tulutsani manja anu kuchokera m'mwamba;ndikwatuleni ndi kundilanditsa kumadzi aakulu,kudzanja la alendo;","amene pakamwa pao alankhula zachabe,ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.","Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu;pa chisakasa cha zingwe khumi ndidzaimbira zakukulemekezani.","Ndiye amene apatsa mafumu chipulumutso:Amene alanditsa Davide mtumiki wake kulupanga loipa.","Ndilanditseni ndi kundipulumutsa kudzanja la alendo,amene pakamwa pao alankhula zachabe,ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.","Kuti ana athu amuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime;ana athu akazi ngati nsanamira za kungodya,zosema zikometsere nyumba ya mfumu.","Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundumitundu;ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwizikwi, inde zikwi khumi kubusako.","Kuti ng'ombe zathu zikhale zosenza katundu;ndi kuti pasakhale kupasula linga kapena kutulukamo,pasakhalenso kufuula m'makwalala athu.","Odala anthu akuona zotere;odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova."]