UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.26 kB
["Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga;ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.","Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu;pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.","Pakuti mdani alondola moyo wanga;apondereza pansi moyo wanga;andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.","Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine;mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga.","Ndikumbukira masiku a kale lomwe;zija mudazichita ndilingirirapo;ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.","Nditambalitsira manja anga kwa Inu:Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.","Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha.Musandibisire nkhope yanu;ndingafanane nao akutsikira kudzenje.","Mundimvetse chifundo chanu mamawa;popeza ndikhulupirira Inu:Mundidziwitse njira ndiyendemo;popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.","Mundilanditse kwa adani anga, Yehova;ndibisala mwa Inu.","Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga;Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.","Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu;mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m'sautso.","Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga,ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga;pakuti ine ndine mtumiki wanu."]