UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 696 B
["Ndifuula nalo liu langa kwa Yehova;ndi mau anga ndipemba kwa Yehova.","Nditsanulira kudandaula kwanga pamaso pake;ndionetsa msauko wanga pamaso pake.","Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga.M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.","Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa;pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.","Ndinafuulira kwa inu, Yehova;ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga,gawo langa m'dziko la amoyo.","Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri;ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andilaka.","Tulutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu;olungama adzandizinga;pakuti mudzandichitira zokoma."]