bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 979 B
JSON
["Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine;munditcherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.","Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu;kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.","Muike mdindo pakamwa panga, Yehova;sungani pakhomo pa milomo yanga.","Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa,kuchita ntchito zoipandi anthu akuchita zopanda pake;ndipo ndisadye zankhuli zao.","Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo:akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu;mutu wanga usakane:Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.","Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe;nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa.","Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda,monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi.","Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye;ndithawira kwa Inu; musataye moyo wanga.","Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo,ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake.","Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao,kufikira nditapitirira ine."]